21
1 “Uwawuze Aisraeli malamulo awa:
Antchito a Chihebri
2 “Mukagula kapolo wa Chihebri, azikugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri muzimumasula, ndipo asalipire kanthu.
3 Ngati anabwera yekha, amasulidwenso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pamene ankabwera, mkaziyo apite nayenso.
4 Ngati bwana wake amupatsa mkazi ndipo mkaziyo anabereka ana aamuna kapena aakazi, mkazi ndi anawo adzakhala a bwanayo ndipo mwamuna yekhayo ndiye adzamasulidwe.
5 “Koma ngati kapoloyo alengeza kuti, ‘Ine sindikufuna kumasulidwa chifukwa ndimakonda mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana,’
6 mbuye wakeyo abwere naye kwa Yehova. Abwere naye pa chitseko kapena pa mphuthu zachitseko ndipo abowole khutu lake ndi chitsulo. Ndipo iye adzakhala kapolo wake moyo wake wonse.
7 “Ngati munthu agulitsa mwana wake wamkazi kukhala mdzakazi, mwanayo asamasulidwe monga achitira ndi akapolo aamuna.
8 Koma ngati mkaziyo sakukondweretsa bwana wake amene wamusankha kuti amukwatire, amulole kuti awomboledwe. Bwanayo alibe mphamvu zomugulitsa kwa anthu achilendo, chifukwa iyeyo waphwanya pangano lake lomukwatira iye.
9 Ngati anamusankha kuti akhale mkazi wa mwana wake, ayenera kumusunga ngati mwana wake wamkazi.
10 Ngati akwatira mkazi wina, asamumane woyambayo chakudya ngakhale chovala ndipo apiritirize kugona naye ngati mkazi wake.
11 Koma ngati sangathe kumuchitira zonsezi, ndiye amuleke apite popanda kulipira kanthu.
Munthu Akapwetekedwa
12 “Munthu aliyense amene amenya mnzake namupha, iyenso ayenera kuphedwa.
13 Koma ngati sanachite dala, ndipo Mulungu analola kuti zichitike, iyeyo athawire ku malo kumene ndidzakupatsani.
14 Koma ngati munthu akonza chiwembu ndi kupha mnzake mwadala, ameneyo muchotseni ngakhale ku guwa langa lansembe ndipo aphedwe.
15 “Munthu aliyense amene amenya abambo ake kapena mayi ake ayenera kuphedwa.
16 “Munthu aliyense amene aba munthu mnzake, ndi kukamugulitsa, kapena kumangomusunga, ayenera kuphedwa.
17 “Aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.
18 “Ngati anthu awiri akangana ndipo wina amenya mnzake ndi mwala kapena nkhonya koma wosamupha, womenyedwayo akadwala nagona pa bedi,
19 kenaka nachira ndi kuyamba kuyenda ndi ndodo kutuluka kunja kwa nyumba yake, ndiye kuti womenya mnzakeyo sadzayimbidwa mlandu. Komabe adzayenera kulipira womenyedwayo chifukwa cha nthawi imene anagona pa bedi ija, ndiponso ayenera kumusala mpaka atachiritsitsa.
20 “Ngati munthu amenya kapolo wake wamwamuna kapena mdzakazi ndi ndodo, kapolo uja ndikufa chifukwa cha kumenyedwako, munthuyo ayenera kulangidwa.
21 Koma ngati kapolo uja akhala ndi moyo tsiku lonse kapena masiku awiri, ndiye kuti mbuye uja asalangidwe chifukwa kapolo ndi chuma chake.
22 “Ngati anthu akumenyana ndi kupweteka mayi woyembekezera, mayiyo napita padera, koma osavulala, wolakwayo ayenera kulipira chilichonse chimene mwamuna wake wa mkaziyo adzalamula ndipo bwalo lamilandu lavomereza.
23 Koma ngati wavulazidwa kwambiri, ndiye malipiro ake adzakhala motere: moyo kulipa moyo,
24 diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, mkono kulipa mkono, phazi kulipa phazi.
25 Kutentha ndi moto kulipa kutentha ndi moto, bala kulipa bala, mkwingwirima kulipa mkwingwirima.
26 “Ngati munthu amenya wantchito wake wa mwamuna kapena mdzakazi wake pa diso ndi kuliwononga, wantchitoyo amasulidwe ngati malipiro a diso lake.
27 Ndipo ngati agulula dzino la wantchito wamwamuna kapena mdzakazi, wantchitoyo amasulidwe ngati malipiro a dzino lake.
28 “Ngati ngʼombe ipha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga yake, iponyedwe miyala ndipo nyama yake isadyedwe. Ndipo mwini ngʼombeyo asayimbidwe mlandu.
29 Koma ngati ngʼombeyo inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwini wakeyo anachenjezedwa koma iye sanayimange ndipo yapha mwamuna kapena mkazi, ngʼombeyo iponyedwe miyala ndipo mwini wakeyo aphedwenso.
30 Koma ngati wauzidwa kuti alipire, iye apereke zimene wauzidwazo kuti awombole moyo wake.
31 Lamulo ili ligwirenso ntchito ngati ngʼombeyo yagunda mwana wamwamuna kapena wamkazi.
32 Ngati ngʼombeyo yagunda kapolo wamwamuna kapena mdzakazi, mwini ngʼombeyo apereke masekeli makumi atatu a siliva kwa mwini kapoloyo, ndipo ngʼombeyo iponyedwe miyala.
33 “Munthu akasiya dzenje lapululu kapena akakumba dzenje koma wosaphimbapo, ndipo ngʼombe kapena bulu nʼkugweramo,
34 mwini dzenjelo amulipire mwini chiweto chakufacho koma iye atenge chiwetocho.
35 “Ngati ngʼombe ya munthu wina ipha ngʼombe ya mnzake, ngʼombe yamoyo ija igulitsidwe ndipo anthu awiriwo agawane pakati ndalama yake. Achite chimodzimodzi ndi ngʼombe yakufa ija.
36 Koma zikadziwika kuti ngʼombeyo inali ndi khalidwe logunda, ndipo mwini wake samayitsekera mʼkhola, mwini ngʼombeyo alipire ngʼombe ina yamoyo koma atenge yakufayo.”