15
Nyimbo ya Mose ndi Miriamu 
 
1 Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi:  
“Ine ndidzayimbira Yehova  
pakuti wakwezeka mʼchigonjetso.  
Kavalo ndi wokwera wake,  
Iye wawaponya mʼnyanja.   
2 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;  
ndiye chipulumutso changa.  
Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda,  
Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza.   
3 Yehova ndi wankhondo;  
Yehova ndilo dzina lake.   
4 Magaleta a Farao ndi asilikali ake ankhondo  
Iye wawaponya mʼnyanja.  
Akatswiri ankhondo amphamvu a Farao  
amizidwa mʼNyanja Yofiira.   
5 Nyanja yakuya inawaphimba;  
Iwo anamira pansi ngati mwala.”   
   
 
6 Yehova, dzanja lanu lamanja  
ndi laulemerero chifukwa cha mphamvu zake.  
Ndithu Yehova, dzanja lanu lamanja  
linaphwanya mdani.   
7 Ndi ulemerero wanu waukulu,  
munagonjetsa okutsutsani.  
Inu munatumiza mkwiyo wanu waukulu;  
ndipo unawapsereza ngati udzu.   
8 Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu  
madzi anawunjikana pamodzi.  
Nyanja yakuya ija inasanduka  
madzi owuma gwaa kufika pansi.   
   
 
9 Mdaniyo anati,  
“Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira.  
Ndidzagawa chuma chawo;  
ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa.  
Ine ndidzasolola lupanga langa,  
ndi mkono wanga ndidzawawononga.”   
10 Koma Inu munawuzira mphepo yanu,  
ndipo nyanja inawaphimba.  
Iwo anamira ngati chitsulo  
mʼmadzi amphamvu.   
   
 
11 Ndithu Yehova, pakati pa milungu,  
ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera,  
ndiponso wotamandika wolemekezeka,  
chifukwa cha ntchito zanu,  
zazikulu ndi zodabwitsa?   
12 Munatambasula dzanja lanu lamanja  
ndipo dziko linawameza.   
   
 
13 Ndi chikondi chanu chosasinthika mudzatsogolera  
anthu amene munawawombola.  
Ndi mphamvu zanu munawatsogolera  
ku malo anu woyera.   
14 Anthu amitundu ina anamva za mbiriyi ndipo ananjenjemera ndi mantha,  
mantha woopsa agwira anthu a dziko la Filisiti.   
15 Tsopano mafumu a ku Edomu agwidwa ndi mantha aakulu,  
otsogolera a dziko la Mowabu akunjenjemera ndi mantha,  
ndipo anthu a ku Kanaani asungunuka ndi mantha.   
16 Onse agwidwa ndi mantha woopsa.  
Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu,  
iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu,  
Inu Yehova atadutsa;  
inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula.   
17 Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa  
pa phiri lanu.  
Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo;  
malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu.   
18 “Yehova adzalamula  
mpaka muyaya.”   
19 Akavalo a Farao, magaleta ndi oyendetsa akavalo atalowa mʼnyanja, Yehova anawabwezera madziwo mʼnyanja ndi kuwamiza, koma Aisraeli anawoloka nyanjayo powuma.  
20 Ndipo Miriamu mneneri wamkazi, mlongo wa Aaroni anatenga zoyimbira ndipo akazi onse anamutsatira pambuyo, akuyimba ndi zoyimbira ndi kuvina.  
21 Miriamu anawayimbira nyimbo iyi:  
“Imbirani Yehova,  
chifukwa iye wapambana.  
Kavalo ndi wokwerapo wake  
Iye wawamiza mʼnyanja.”   
Madzi a ku Mara ndi Elimu 
 
22 Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi.  
23 Ndipo anafika ku Mara. Koma sanathe kumwa madzi akumeneko chifukwa anali owawa. (Ndi chifukwa chake malowo amatchedwa Mara).  
24 Tsono anthu aja anadandaulira Mose ndi kumufunsa kuti, “Kodi tikumwa chiyani?”   
25 Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino.  
Kumeneko Yehova anawayikira lamulo ndi maweruziro. Kumenekonso Yehova anawayesa.  
26 Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”   
27 Kenaka anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi awiri, ndipo anamanga misasa yawo kumeneko pafupi ndi madzi.