10
Anthu Avomereza Tchimo Lawo
Pamene Ezara ankapemphera ndi kuvomereza tchimo lawo, akulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, anthu ambiri anabwera kwa iye kudzasonkhana naye. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera mʼdziko lonse la Israeli ndipo ankalira kwambiri. Ndipo Sekaniya, mwana wa Yehieli, wa fuko la Elamu, anawuza Ezara kuti, “Ife takhala osakhulupirika kwa Mulungu wathu ndipo takhala tikukwatira akazi achilendo a mayiko akunowa. Koma ngakhale zili chomwechi, chikhulupiriro chilipobe pakati pa Aisraeli. Tsopano tiyeni tichite naye pangano Mulungu wathu, kuti tichotse akazi onsewa ndi ana awo, potsata malangizo a inu mbuye wanga ndi wa anthu amene amaopa malamulo a Mulungu wathu. Lolani kuti zichitike motsatira malamulo. Tsono dzukani, imeneyi ndi ntchito yanu. Ife tikuthandizani. Limbani mtima ndipo gwirani ntchitoyi.”
Choncho Ezara anayimirira ndipo analumbiritsa akulu a ansembe, Alevi ndi Aisraeli onse, kuti adzachitedi monga Sekaniya ananenera. Tsono onse analumbira. Ezara anachoka ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu. Anatandala kumeneko usiku wonse ndipo sanadye chakudya kapena kumwa madzi popeza ankalira chifukwa cha kusankhulupirika kwa anthu obwera ku ukapolo.
Tsono anthu analengeza mʼdziko lonse la Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Yerusalemu kwa onse ochokera ku ukapolo aja kuti asonkhane ku Yerusalemu. Ananena kuti wina aliyense amene saonekera pakutha pa masiku atatu, adzalandidwa katundu wake, potsata malangizo a nduna ndi akuluakulu, ndipo adzachotsedwa mʼgulu la anthu obwerako ku ukapolo.
 
Choncho anthu onse a mʼdziko la Yuda ndi a mʼdziko la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu asanathe masiku atatu. Limeneli linali tsiku la 20 la mwezi wa 9. Anthu onse anakhala pansi pa bwalo la Nyumba ya Mulungu akunjenjemera chifukwa cha mvula yambiri imene inagwa. 10 Ndipo wansembe Ezara anayimirira nawuza anthuwo kuti, “Inu mwachimwa pomakwatira akazi achikunja ndi kumawonjezera pa tchimo la Aisraeli. 11 Tsopano lapani kwa Yehova, Mulungu wa makolo anu ndi kuchita zimene akufuna. Dzipatuleni kwa anthu a mayiko enawa ndi kwa akazi achikunjawa.”
12 Gulu lonse la anthu linayankha ndi mawu ofuwula kuti, “Nʼzoona! Tichita monga mwaneneramu. 13 Koma pano pali anthu ambiri ndiponso mvula ikugwa kwambiri, choncho sitingakayime panja. Ndiponso ntchitoyi si ya tsiku limodzi kapena awiri, chifukwa tachimwa kwambiri pa zimene tachitazi. 14 Tsono mulole kuti atsogoleri athu ayimirire mʼmalo mwa anthu onse. Aliyense wa mʼmizinda yathu amene anakwatira mkazi wachikunja abwere pa nthawi imene inu munene, ndipo abwere pamodzi ndi akuluakulu ndi oweruza a mzindawo. Choncho mkwiyo wa Mulungu wathu udzatichoka.” 15 Koma Yonatani yekha mwana wa Asaheli ndi Yahazieli mwana wa Tikiva ndiwo anatsutsapo pa zimenezi. Tsono Mesulamu ndi Mlevi Sebetai anawayikira kumbuyo.
16 Choncho anthu obwerako ku ukapolo aja anachita zimene zimafunika. Ndipo wansembe Ezara anasankha amuna amene anali atsogoleri a mabanja potsata mafuko awo ndipo onsewo analembedwa mayina awo. Tsiku loyamba la mwezi wa khumi anayambapo kuyifufuza nkhani imeneyi. 17 Ndipo pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba anali atathana nawo anthu amene anakwatira akazi achilendo aja.
Okwatira Akazi Achilendo
18 Nawu mʼndandanda wa ansembe amene anakwatira akazi achikunja:
 
Pa banja la Yesuwa ndi abale ake, ana a Yozadaki, panali awa: Maaseiya, Eliezara, Yaribu ndi Gedaliya. 19 Iwo anatsimikiza zochotsa akazi awo ndipo chifukwa cha kulakwa kwawo aliyense anapereka nkhosa yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo.
20 Pa banja la Imeri panali awa:
Hanani ndi Zebadiya.
21 Pa banja la Harimu panali awa:
Maseya, Eliya, Semaya, Yehieli ndi Uziya.
22 Pa banja la Pasuri panali awa:
Eliyoenai, Maseya, Ismaeli, Netaneli, Yozabadi ndi Eleasa.
 
23 Pakati pa Alevi panali:
 
Yozabadi, Simei, Kelaya (ndiye kuti, Kelita). Petaya, Yuda ndi Eliezara.
24 Pakati pa oyimba nyimbo panali
Eliyasibu.
Ochokera kwa alonda a zipata:
Salumu, Telemu ndi Uri.
 
25 Ochokera pakati pa Aisraeli ena:
 
a fuko la Parosi anali
Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eliezara, ndi Benaya.
26 A fuko la Elamu anali
Mataniya, Zekariya, Yehieli, Abidi, Yeremoti ndi Eliya.
27 A fuko la Zatu anali
Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi ndi Aziza.
28 A fuko la Bebai anali
Yehohanani, Hananiya, Zabayi ndi Atilayi.
29 A fuko la Bani anali
Mesulamu, Maluki, Adaya, Yasubu, Seali ndi Yeremoti.
30 A fuko la Pahati-Mowabu anali
Adina, Kelali, Benaya, Maseya, Mataniya, Bezaleli, Binuyi ndi Manase.
31 A fuko la Harimu anali
Eliezara, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni, 32 Benjamini, Maluki ndi Semariya.
33 A fuko la Hasumu anali
Mataneyi, Matata, Zabadi, Elifeleti, Yeremayi, Manase ndi Simei.
34 A fuko la Bani anali
Madai, Amramu, Uweli, 35 Benaya, Bediya, Keluhi, 36 Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, 37 Mataniya, Matenayi ndi Yasu.
38 A fuko la Binuyi anali
Simei, 39 Selemiya, Natani, Adaya, 40 Makinadebayi, Sasai, Sarai, 41 Azaleli, Selemiya, Semariya, 42 Salumu, Amariya ndi Yosefe.
43 A fuko la Nebo anali
Yeiyeli, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yoweli ndi Benaya.
 
44 Onsewa anakwatira akazi achilendo. Tsono anawasudzula akaziwo ndi kuwatumiza kwawo pamodzi ndi ana awo.