7
Chimaliziro Chafika
Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti, “Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuwuza dziko la Israeli kuti:
“Chimaliziro! Chimaliziro chafika
ku ngodya zinayi za dziko.
Chimaliziro chili pa iwe tsopano.
Mkwiyo wanga ndidzawuthira pa iwe.
Ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako
ndi kukulanga chifukwa cha zonyansa zako.
Ine sindidzakumvera chisoni
kapena kukuleka.
Ndidzakulanga ndithu chifukwa cha ntchito zako zoyipa
komanso chifukwa cha miyambo yako yonyansa imene ili pakati pako.
Pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
 
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi:
“Chiwonongeko! Chiwonongeko chimene sichinamvekepo!
Taona chikubwera!
Chimaliziro chafika!
Chimaliziro chafika!
Chiwonongeko chakugwera.
Taona chafika!
Inu anthu okhala mʼdziko,
chiwonongeko chakugwerani.
Nthawi yafika, tsiku layandikira; tsiku la chisokonezo osati la chimwemwe pa mapiri.
Ine ndili pafupi kukukwiyirani,
ndipo ukali wanga udzathera pa iwe;
Ine ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako
ndiponso ndidzakulanga chifukwa cha miyambo yako yonyansa.
Ine sindidzakumvera chisoni
kapena kukuleka.
Ndidzakulanga malingana ndi ntchito zako
ndiponso chifukwa cha miyambo yako yonyansa pakati pako.
‘Pamenepo udzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndimakantha.’
 
10 “Taona, tsikulo!
Taona, lafika!
Chiwonongeko chako chabwera.
Ndodo yaphuka mphundu za maluwa.
Kudzitama kwaphuka.
11 Chiwawa chasanduka ndodo
yowakwapulira chifukwa cha kuyipa kwawo.
Palibe mwa anthu amenewo amene adzatsale.
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa unyinji wawo.
Palibiretu ndipo sipadzapezeka
munthu wowalira maliro.
12 Nthawi yafika!
Tsiku layandikira!
Munthu wogula asakondwere
ndipo wogulitsa asamve chisoni,
popeza ukali wanga uli pa gulu lonse.
13 Wogulitsa sadzazipezanso zinthu
zimene anagulitsa kwa wina
chinkana onse awiri akanali ndi moyo,
pakuti chilango chidzagwera onsewo
ndipo sichingasinthike.
Chifukwa cha machimo awo, palibe aliyense
amene adzapulumutsa moyo wake.
 
14 “Lipenga lalira,
ndipo zonse zakonzeka.
Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo,
pakuti mkwiyo wanga uli pa gulu lonse.
15 Ku bwalo kuli kumenyana
ndipo mʼkati muli mliri ndi njala.
Anthu okhala ku midzi
adzafa ndi nkhondo.
Iwo okhala ku mizinda
adzafa ndi mliri ndi njala.
16 Onse amene adzapulumuka
ndi kumakakhala ku mapiri,
azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa.
Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake.
17 Dzanja lililonse lidzalefuka,
ndipo bondo lililonse lidzalobodoka ngati madzi.
18 Iwo adzavala ziguduli
ndipo adzagwidwa ndi mantha.
Adzakhala ndi nkhope zamanyazi
ndipo mitu yawo adzameta mpala.
 
19 “Iwo adzataya siliva wawo mʼmisewu
ndipo golide wawo adzakhala chinthu chonyansa.
Siliva ndi golide wawo
sizidzatha kuwapulumutsa
pa tsiku la ukali wa Yehova.
Chuma chawochi sichidzawathandiza kuthetsa njala,
kapena kukhala okhuta,
pakuti ndicho chinawagwetsa mʼmachimo.
20 Iwo ankanyadira zodzikongoletsera zawo zamakaka
ndipo ankazigwiritsa ntchito kupanga mafano awo onyansa ndi zonyansa zawo zina.
Nʼchifukwa chake Ine ndidzazisandutsa
kukhala zowanyansa.
21 Ndidzazipereka kwa alendo kuti azifunkhe.
Anthu oyipa a dziko lapansi adzazilanda
ndi kudziyipitsa.
22 Ine ndidzawalekerera anthuwo
ndipo adzayipitsa malo anga apamtima.
Adzalowamo ngati mbala
ndi kuyipitsamo.
 
23 “Konzani maunyolo,
chifukwa dziko ladzaza ndi anthu opha anzawo
ndipo mzinda wadzaza ndi chiwawa.
24 Ndidzabweretsa mitundu ya anthu oyipitsitsa
kuti idzalande nyumba zawo.
Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu
pamene anthu akunja adzalowa mʼmalo awo achipembedzo ndi kuyipitsamo.
25 Nkhawa ikadzawafikira
adzafunafuna mtendere koma osawupeza.
26 Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake,
ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake.
Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri.
Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo,
ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.
27 Mfumu idzalira,
kalonga adzagwidwa ndi mantha.
Manja a anthu a mʼdzikomo azidzangonjenjemera ndi mantha.
Ine ndidzawalanga molingana ndi machitidwe awo,
ndipo ndidzawaweruza molingana ndi momwe anaweruzira anzawo.
Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”