46
1 “Ambuye Yehova akuti, Chipata chakummawa cha bwalo lamʼkati chizikhala chotseka pa masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito, koma chizitsekulidwa pa tsiku la sabata ndi pa tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano.
2 Mfumu izilowa podzera mʼkhonde la mʼkati la chipata pochokera kunja, nʼkudzayima pafupi ndi nsanamira yapakhomo. Ansembe apereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yachiyanjano. Mfumuyo ipembedze pa chiwundo cha pa chipatacho kenaka nʼkutuluka. Koma chipatacho asachitseke mpaka madzulo.
3 Anthu a mʼdziko azipembedza pamaso pa Yehova pa khomo la chipata chimenechi pa masiku a sabata ndi pa tsiku la mwezi watsopano.
4 Nsembe yopsereza imene mfumu iyenera kupereka kwa Yehova ikhale motere: pa tsiku la Sabata izipereka ana ankhosa aamuna asanu ndi mmodzi wopanda chilema, ndiponso nkhosa yayima yopanda chilema.
5 Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, mfumu izipereka nsembe ya chakudya yokwanira efa imodzi. Pamodzi ndi ana ankhosa, mfumu izipereka monga ikufunira kutero. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse ya tirigu.
6 Pa tsiku la mwezi watsopano mfumuyo ipereke mwana wangʼombe wamwamuna, ana ankhosa asanu ndi mmodzi ndiponso nkhosa yayimuna, zonsezi zopanda chilema.
7 Ipereke efa imodzi ya tirigu pa ngʼombe yayimuna iliyonse ndiponso efa ina pa nkhosa yayimuna iliyonse. Pa ana ankhosa ipereke tirigu monga ikufunira kutero. Pamodzi ndi efa ya tirigu, ipereke hini imodzi ya mafuta.
8 Pamene mfumu ikulowa, izidzera mʼkhonde lamʼkati la chipata chakummawa, izitulukiranso pomwepo.
9 “Anthu a mʼdzikomo akabwera kudzapembedza Yehova pa masiku a chikondwerero, ngati munthu alowera pa chipata chakumpoto atulukire chipata chakummwera. Munthu wolowera chipata chakummwera, atulukire chipata chakumpoto. Munthu asatulukire pomwe walowera, koma atulukire pa chipata choyangʼanana nacho.
10 Mfumu izidzakhala pakati pawo. Anthu akamadzalowa mfumu idzalowa nawo. Anthu akamadzatuluka mfumu idzatuluka nawo.
11 “Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za chakudya zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, efa imodzinso ndi nkhosa yayimuna, koma pa mwana wankhosa apereke monga angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse.
12 Pamene mfumu ikufuna kupereka chopereka chaufulu kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena zopereka za chiyanjano, ayitsekulire chipata chakummawa. Iyo ipereke nsembe yopsereza kapena zopereka zake za chiyanjano monga imachitira pa tsiku la Sabata. Kenaka ituluke ndipo mfumuyo itatuluka, atseke chitsekocho.
13 “Tsiku lililonse nthawi ya mmawa azipereka kwa Yehova mwana wankhosa wa chaka chimodzi.
14 Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso mmawa uliwonse chopereka cha chakudya chokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Chopereka cha chakudya chimenechi chiziperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mwa lamulo.
15 Motero azipereka mwana wankhosa ndi chopereka cha chakudya ndi mafuta mmawa uliwonse kuti zikhale nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku.
16 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ngati kalonga apereka mphatso chigawo cha cholowa chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo idzakhala ya ana akewo. Idzakhala yawo chifukwa ndi cholowa chawo.
17 Koma ngati ipereka mphatso yotere kuchokera pa cholowa chake kwa mmodzi mwa antchito ake, mphatsoyo idzakhala ya wantchitoyo mpaka chaka chaufulu. Pambuyo pake idzabwereranso kwa kalongayo chifukwa cholowa chake ndi cha ana ake.
18 Kalonga asalande cholowa chilichonse cha anthu, kuwachotsa mʼdera lawo la dziko. Iye apereke kwa ana ake cholowa chawo chochokera pa chuma chakechake, kuti pasapezeke ndi mmodzi yemwe mwa anthu anga wolandidwa chuma chake.’ ”
19 Kenaka munthu uja anandidzeretsa pa khomo la pambali pa chipata nandilowetsa ku zipinda za ansembe zoyangʼana kumpoto. Ndipo ndinaona kumeneko malo chakumadzulo kwa zipindazo.
20 Munthuyo anandiwuza kuti, “Awa ndi malo amene ansembe adzaphikirapo nsembe yopepesera kupalamula ndi nsembe yopepesera machimo. Kumenekonso azidzawotcherako chopereka cha chakudya. Sadzatuluka nazo zoyerazi mʼbwalo lakunja kuopa kuti angapatsireko kuyera anthu ena.”
21 Pambuyo pake anandilowetsa mʼbwalo lakunja napita nane ku ngodya zinayi za bwalolo. Ndipo ndinaona mʼkati mwa ngodya iliyonse bwalo lina.
22 Motero pa ngodya zinayi za bwalo panalinso mabwalo ena angʼonoangʼono. Mabwalo amenewa anali ofanana. Mulitali mwake munali mamita makumi awiri ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi ndi asanu.
23 Kuzungulira mabwalo anayi angʼonoangʼono aja panali mpanda wamiyala, ndi malo asonkhapo moto omangidwa mʼmunsi mwa mpandawo mozungulira.
24 Munthuyo anandiwuza kuti, “Izi ndi zipinda zophikiramo. Mʼmenemu anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzaphikiramo nyama za nsembe za anthu.”