32
Nyimbo ya Maliro a Farao
1 Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiwiri, chaka chakhumi ndi chiwiri, Yehova anandiyankhula kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu imba nyimbo ya maliro a Farao mfumu ya Igupto ndipo uyiwuze kuti,
“Iwe umadziyesa ngati mkango pakati pa mitundu ya anthu.
Koma iwe uli ngati ngʼona mʼnyanja.
Umakhuvula mʼmitsinje yako,
kuvundula madzi ndi mapazi ako
ndi kudetsa madzi mʼmitsinje.
3 “Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Pogwiritsa ntchito gulu la anthu a mitundu yambiri,
ndidzakuponyera khoka langa
ndi kukugwira mu ukonde wanga.
4 Ndidzakuponya ku mtunda
ndi kukutayira pansi.
Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe,
ndipo zirombo zonse za dziko lapansi zidzakudya.
5 Ndidzayanika mnofu wako pa mapiri
ndipo zigwa zidzadzaza ndi zotsalira zako.
6 Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako,
mpaka kumapiri komwe,
ndipo mitsinje idzadzaza ndi mnofu wako.
7 Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba miyamba
ndikudetsa nyenyezi zake.
Ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo,
ndipo mwezi sudzawala.
8 Zowala zonse zamumlengalenga
ndidzazizimitsa;
ndidzachititsa mdima pa dziko lako,
akutero Ambuye Yehova.
9 Ndidzasautsa mitima ya anthu a mitundu yambiri
pamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,
ku mayiko amene iwe sunawadziwe.
10 Ine ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yambiri adabwe nawe,
ndipo mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha aakulu chifukwa cha iwe
pamene ndidzaonetsa lupanga langa pamaso pawo.
Pa nthawi ya kugwa kwako,
aliyense wa iwo adzanjenjemera
moyo wake wonse.
11 “ ‘Pakuti ndikunena Ine Ambuye Yehova kuti,
“ ‘Lupanga la mfumu ya ku Babuloni
lidzabwera kudzalimbana nawe.
12 Ndidzachititsa gulu lako lankhondo kuti ligwe
ndi lupanga la anthu amphamvu,
anthu ankhanza kwambiri pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Adzathetsa kunyada kwa Igupto,
ndipo gulu lake lonse la nkhondo lidzagonjetsedwa.
13 Ndidzawononga ziweto zake zonse
zokhala mʼmbali mwa madzi ambiri.
Ku madziko sikudzaonekanso phazi la munthu
kapena kudetsedwa ndi phazi la ziweto.
14 Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi ake
ndipo mitsinje yake idzayenda mokometsera ngati mafuta,
akutero Ambuye Yehova.
15 Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja;
ndikadzawononga dziko lonse
ndi kukantha onse okhala kumeneko,
adzadziwa kuti ndine Yehova.’
16 “Mawu angawa adzakhala nyimbo ya maliro. Ana a akazi amitundu ya anthu adzayimba, kuyimbira Igupto ndi gulu lake lonse la nkhondo, akutero Ambuye Yehova.”
17 Pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiwiri, Yehova anayankhula kuti:
18 “Iwe mwana wa munthu, lirira gulu lankhondo la Igupto ndipo uwalowetse pamodzi ndi anthu ena amphamvu a mayiko ena ku dziko la anthu akufa.
19 Ufunse kuti, ‘Ndani amene akukuposa kukongola? Tsikirani ku manda ndi kukhala pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe.’
20 Aigupto adzagwa pakati pa amene akuphedwa ndi lupanga. Lupanga ndi losololedwa kale. Iye adzaphedwa pamodzi ndi gulu lake lankhondo.
21 Mʼkati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana za Igupto nʼkumati, ‘Afika kuno anthu osachita mdulidwe aja! Ndi awa agona apawa, ophedwa pa nkhondo.’
22 “Asiriya ali komweko ndipo ankhondo ake onse ali mʼmanda omuzungulira. Onsewo anaphedwa pa nkhondo.
23 Manda awo ali kumalo ozama a dzenje, ndipo ankhondo ake azungulira manda ake. Onse amene anaopseza dziko la anthu amoyo aphedwa, agwa ndi lupanga.
24 “Elamu ali komweko ndipo ankhondo ake ali mʼmanda omuzungulira. Onsewa anaphedwa pa nkhondo, natsikira ku manda ali osachita mdulidwe. Iwowa kale ankaopseza anthu pa dziko lapansi. Tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda.
25 Amukonzera pogona pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse la nkhondo litazungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe ophedwa ndi lupanga. Paja anthuwa ankaopsa mʼdziko la anthu a moyo. Koma tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Iwo ayikidwa pakati pa anthu ophedwa.
26 “Mesaki ndi Tubala ali komweko, pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo litazungulira manda awo. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe, ophedwa ndi lupanga. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo.
27 Iwo sanayikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene anatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zawo zomwe za nkhondo. Malupanga awo anawayika ku mitu yawo, ndipo zishango zawo anaphimba mafupa awo. Kale anthu amphamvu amenewa ankaopsa dziko la anthu amoyo.
28 “Iwenso Farao, udzaphwanyidwa ndi kuyikidwa pakati pa anthu osachita mdulidwe, amene anaphedwa ndi lupanga.
29 “Edomu ali kumeneko pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, koma anayikidwa. Ayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje.
30 “Akalonga onse akumpoto pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni ali kumeneko. Anatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi ngakhale anali owopsa ndi mphamvu zawo. Iwo akugona osachita mdulidwe pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga ndipo akuchita manyazi pamodzi ndi iwo amene anatsikira kale ku manda.
31 “Farao ndi gulu lake lankhondo akadzawaona iwowa adzathunza mtima pokumbukira kuchuluka kwa gulu lake lankhondo limene linaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
32 Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. Koma Faraoyo pamodzi ndi ankhondo ake onse adzayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi amene anaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”