30
Za Kulangidwa kwa Igupto
1 Yehova anandiyankhula kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.
“ ‘Ufuwule mawu awa akuti,
‘Kalanga, tsiku lafika!’
3 Pakuti tsiku layandikira,
tsiku la Yehova lili pafupi,
tsiku la mitambo yakuda,
tsiku lachiwonongeko cha mitundu ya anthu.
4 Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto
ndipo mavuto adzafika pa Kusi.
Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto,
chuma chake chidzatengedwa
ndipo maziko ake adzagumuka.
5 Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto.
6 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:
“ ‘Onse othandiza Igupto adzaphedwa
ndipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu.
Adzaphedwa ndi lupanga
kuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’ ”
ndikutero Ine Ambuye Yehova.
7 “ ‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinja
kupambana mabwinja ena onse opasuka,
ndipo mizinda yake idzakhala yopasuka
kupambana mizinda ina yonse.
8 Nditatha kutentha Igupto
ndi kupha onse omuthandiza,
pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
9 “ ‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.
10 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndidzagwiritsa ntchito Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni
kuti ndithetse gulu lankhondo la Igupto.
11 Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja
adzabwera kudzawononga dzikolo.
Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Igupto
ndipo dziko lidzadzaza ndi mitembo.
12 Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo
ndi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa.
Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolo
pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.
Ine Yehova ndayankhula.
13 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndidzawononga mafano
ndi kuthetsa milungu yosema ya ku Mefisi.
Simudzakhalanso mfumu mu Igupto,
ndipo ndidzaopseza dziko lonse.
14 Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi,
ndi kutentha mzinda wa Zowani.
Ndidzalanga mzinda wa Thebesi.
15 Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu,
linga lolimba la Igupto,
ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.
16 Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto;
Peluziumu adzazunzika ndi ululu.
Malinga a Thebesi adzagumuka,
ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi.
17 Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti
adzaphedwa ndi lupanga
ndipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo.
18 Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima
pamene ndidzathyola goli la Igupto;
motero kunyada kwake kudzatha.
Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda,
ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo.
19 Kotero ndidzalanga dziko la Igupto,
ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Farao Watha Mphamvu
20 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti:
21 “Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga.
22 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake.
23 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri.
24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo.
25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto.
26 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”