26
Za Chilango cha Turo
1 Pa chaka cha khumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, Yehova anandiyankhula kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Turo ananyogodola Yerusalemu kuti ‘Hii! Uja amene anali chipata choloweramo anthu a mitundu ina wawonongeka. Zitseko zake zatsekukira ife. Tidzalemera popeza wasanduka bwinja.’
3 Nʼchifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulangani, inu anthu a ku Turo. Ndidzakuyitanirani anthu a mitundu ina kuti adzakulangeni monga momwe mafunde amawombera pa Nyanja.
4 Anthuwo adzawononga makoma a Turo ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake ndipo ndidzamusandutsa thanthwe losalala.
5 Udzakhala poyanikapo makoka pakati pa nyanja. Ine Ambuye Yehova ndayankhula zimenezo. Udzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina.
6 Anthu okhala ku mtunda adzasakazidwa ndi lupanga. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
7 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Iwe Turo, ndidzakubweretsera Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto pamodzi ndi akavalo ndiponso magaleta, anthu okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo.
8 Anthu okhala ku mtunda adzawapha ndi lupanga. Adzapanga mitumbira yankhondo ndi kukukwezera zishango kuti alimbane nawe.
9 Adzagwetsa makoma ako ndi zida zogumulira khoma ndi kugwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake.
10 Akavalo ake adzakhala ochuluka kwambiri kotero kuti adzakukwirira ndi fumbi lawo. Makoma ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo, ngolo ndi magaleta pamene iye adzalowa pa zipata monga mmene amalowera mu mzinda umene makoma ake agwetsedwa.
11 Akavalo ake adzapondaponda mʼmisewu yako yonse ndi ziboda zawo. Adzapha anthu ako ndi lupanga. Mizati yako yolimba idzagwetsedwa.
12 Iwo adzafunkha chuma chako ndipo adzalanda zinthu zako za malonda. Adzagwetsa makoma ako ndi kuwononga nyumba zako zabwino. Adzaponya miyala yako, matabwa ako ndi dothi lako mʼnyanja.
13 Choncho ndidzathetsa phokoso la nyimbo zanu, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso.
14 Ndidzakusandutsa thanthwe losalala, ndipo udzakhala malo woyanikapo makoka a nsomba. Sudzamangidwanso, pakuti Ine Yehova ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.
15 “Ine Ambuye Yehova ndikukuwuza, iwe mzinda wa Turo, kuti zilumba zidzagwedezeka pakumva za kugwa kwako ndiponso poona anthu opweteka akubuwula ndipo anthu akuphedwa pakati pako.
16 Pamenepo mafumu a mʼmbali mwa nyanja adzatsika pa mipando yawo yaufumu. Adzayika pambali mikanjo yawo ndi kuvala zovala zawo zamakaka. Adzachita mantha ndipo adzakhala pansi akunjenjemera kosalekeza. Adzathedwa nzeru poona zimene zakugwera.
17 Pamenepo adzayimba nyimbo yokudandaula ndipo adzati kwa iwe:
“ ‘Nʼkuchita kuwonongeka chotere, iwe mzinda wotchuka,
wodzaza ndi anthu a ku nyanja!
Unali wamphamvu pa nyanja,
iwe ndi nzika zako;
unkaopseza anthu onse amene
ankakhala kumeneko.
18 Tsopano mayiko a mʼmbali mwa nyanja akunjenjemera
chifukwa cha kugwa kwako;
okhala pa zilumba nawonso agwidwa ndi mantha aakulu
chifukwa cha kugwa kwako.’
19 “Mawu a Ine Ambuye Yehova ndi awa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mizinda imene anthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama a mʼnyanja, madzi amphamvu woti akumize.
20 Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ine ndidzakusunga ku dzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene anafa kale motero sudzabwererako kukhala pakati pa anthu amoyo.
21 Ine ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna, koma sudzapezekanso, akutero Ambuye Yehova.”