15
Yerusalemu, Mtengo Wamphesa Wosabereka
1 Yehova anayankhulanso nane kuti,
2 “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wamphesa umapambana bwanji mtengo wina uliwonse? Nthambi zake zimapambana bwanji nthambi ina iliyonse.
3 Mtengo umene uja nʼkupangira chiyani? Kodi anthu angathe kupangira chikhomo chokolekapo zinthu zawo?
4 Taonani, ndi nkhuni chabe zosonkhera moto. Ukaponyedwa pa moto monga nkhuni ndi kuyaka mbali zonse ndi kusanduka makala, kodi ungagwiritsidwe ntchito ina iliyonse?
5 Ngati pamene unali wosapsa sukanatheka kuwugwiritsa ntchito, nanga bwanji utapserera ndi moto, adzawugwiritsa ntchito bwanji?
6 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mtengo wamphesa ndidzawuponya mʼmoto monga ndimachitira ndi mitengo ina ya ku nkhalango. Momwemonso ndidzachita ndi anthu a ku Yerusalemu.
7 Ndidzawalanga pamenepo ngakhale iwo atuluka pa moto, motowo udzawatenthabe. Ndipo pamene ndidzatsutsana nawo, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
8 Ine ndidzasandutsa dziko kukhala chipululu chifukwa anthu akhala osakhulupirika, akutero Ambuye Yehova.’ ”