12
1 Uzikumbukira mlengi wako
masiku a unyamata wako,
masiku oyipa asanafike,
nthawi isanafike pamene udzanena kuti,
“Izi sizikundikondweretsa.”
2 Nthawi ya ukalamba wako, dzuwa ndi kuwala,
mwezi ndi nyenyezi zidzada.
Mitambo idzabweranso mvula itagwa.
3 Nthawi imene manja ako adzanjenjemera,
miyendo yako idzafowoka,
pamene mano ako adzalephera kutafuna chifukwa ndi owerengeka,
ndipo maso ako adzayamba kuchita chidima.
4 Makutu ako adzatsekeka,
ndipo sudzamva phokoso lakunja;
sudzamvanso kusinja kwa pa mtondo
kapena kulira kwa mbalame mmawa.
5 Imeneyi ndiyo nthawi imene anthu amaopa kupita kumalo okwera,
amaopa kuyenda mʼmisewu;
Mutu umatuwa kuti mbuu,
amayenda modzikoka ngati ziwala
ndipo chilakolako chimatheratu.
Nthawi imeneyo munthu amapita ku nyumba yake yamuyaya
ndipo anthu olira maliro amayendayenda mʼmisewu.
6 Kumbukira Iye chingwe cha siliva chisanaduke,
kapena mbale yagolide isanasweke;
mtsuko usanasweke ku kasupe,
kapena mkombero usanathyoke ku chitsime.
7 Iyi ndi nthawi imene thupi lidzabwerera ku dothi, kumene linachokera,
mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene anawupereka.
8 “Zopanda phindu! Zopandapake!” akutero Mlaliki.
“Zonse ndi zopandapake!”
Mawu Otsiriza
9 Mlaliki sanali wozindikira zinthu kokha ayi, komanso ankaphunzitsa anthu. Iye ankasinkhasinkha ndi kufufuzafufuza ndi kulemba mwadongosolo miyambi yambiri.
10 Mlaliki anafufuzafufuza kuti apeze mawu oyenera, ndipo zimene analemba zinali zolondola ndiponso zoona.
11 Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga, zokamba zawo zimene anasonkhanitsa zili ngati misomali yokhomera, yoperekedwa ndi mʼbusa mmodzi.
12 Samalira mwana wanga, za kuwonjezera chilichonse pa zimenezi.
Kulemba mabuku ambiri sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi.
13 Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa:
uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake,
pakuti umenewu ndiwo udindo
wa anthu onse.
14 Pakuti Mulungu adzaweruza zochita zonse,
kuphatikizanso zinthu zonse zobisika,
kaya zabwino kapena zoyipa.