9
Israeli Adzawonongedwa 
 
1 Ine ndinaona Ambuye atayima pambali pa guwa lansembe, ndipo anati:  
“Kantha mitu ya nsanamira  
kuti ziwundo za nyumba zigwedezeke.  
Muzigwetsere pa mitu ya anthu onse,  
onse amene atsalira ndidzawapha ndi lupanga.  
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathawe,  
palibe amene adzapulumuke.   
2 Ngakhale atakumba pansi mpaka ku malo a anthu akufa,  
dzanja langa lidzawatulutsa kumeneko.  
Ngakhale atakwera kumwamba  
Ine ndidzawatsakamutsa kumeneko.   
3 Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli,  
Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira.  
Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu,  
ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko.   
4 Ngakhale adani awo awakusire ku ukapolo,  
ndidzalamula lupanga kuti liwaphe kumeneko.  
Ndidzawayangʼanitsitsa  
kuti zoyipa ziwagwere; osati zabwino.”   
   
 
5 Ambuye Yehova Wamphamvuzonse  
amene amakhudza dziko lapansi ndipo dzikolo limasungunuka,  
onse amene amakhala mʼmenemo amalira.  
Dziko lonse lidzadzaza ngati mtsinje wa Nailo,  
kenaka nʼkuphwera ngati mtsinje wa ku Igupto.   
6 Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba,  
ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi,  
Iye amene amayitana madzi a ku nyanja  
ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi,  
dzina lake ndiye Yehova.   
   
 
7 “Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simuli  
chimodzimodzi ndi Akusi?”  
Akutero Yehova.  
“Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto,  
Afilisti ku Kafitori  
ndi Aaramu ku Kiri?   
   
 
8 “Taonani, maso a Ambuye Yehova  
ali pa ufumu wochimwawu.  
Ndidzawufafaniza  
pa dziko lapansi.  
Komabe sindidzawononga kotheratu  
nyumba ya Yakobo,”  
akutero Yehova.   
9 “Pakuti ndidzalamula,  
ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israeli  
pakati pa mitundu yonse ya anthu  
monga momwe amasefera ufa mʼsefa,  
koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi.   
10 Anthu onse ochimwa pakati pa anthu anga  
adzaphedwa ndi lupanga,  
onse amene amanena kuti,  
‘Tsoka silidzatigwera ife kapena kutiwononga.’   
Kubwezeretsedwa kwa Israeli 
 
11 “Tsiku limenelo ndidzabwezeretsa  
nyumba ya Davide imene inagwa.  
Ndidzakonzanso malo amene anagumuka,  
ndi kuyimanganso  
monga inalili poyamba,   
12 kuti adzatengenso otsala a Edomu  
ndi mitundu yonse imene imatchedwa ndi dzina langa,”  
akutero Yehova amene adzachita zinthu izi.   
13 Yehova akunena kuti  
“Nthawi ikubwera pamene mlimi wotipula adzapyola wokolola  
ndipo woponda mphesa adzapyola wodzala mbewu.  
Mapiri adzachucha vinyo watsopano  
ndi kuyenderera pa zitunda zonse.   
14 Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli;  
mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo.  
Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake;  
adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.   
15 Ndidzakhazika Aisraeli mʼdziko mwawo,  
ndipo sadzachotsedwamonso mʼdziko  
limene Ine ndawapatsa,”  
   
 
akutero Yehova Mulungu wako.