5
Mawu Odandawulira Aisraeli 
 
1 Israeli, imva mawu awa, nyimbo ya maliro imene ndikuyimba za iweyo:   
2 “Namwali Israeli wagwa,  
moti sadzadzukanso,  
wasiyidwa mʼdziko lake lomwe,  
popanda woti ndi kumudzutsa.”   
3 Ambuye Yehova akuti,  
“Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu  
udzatsala ndi anthu 100 okha;  
mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu  
udzatsala ndi anthu khumi okha basi.”   
4 Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi:  
“Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo;   
5 musafunefune Beteli,  
musapite ku Giligala,  
musapite ku Beeriseba.  
Pakuti Giligala adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo,  
ndipo Beteli adzawonongekeratu.”   
6 Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo,  
mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto;  
motowo udzawononga,  
ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli.   
   
 
7 Inu amene mumasandutsa chiweruzo cholungama kukhala chowawa  
ndi kunyoza chilungamo.   
8 (Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana,  
amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa  
ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku,  
amene amayitana madzi a mʼnyanja  
ndi kuwathira pa dziko lapansi,  
Yehova ndiye dzina lake.   
9 Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu  
ndi kuwononga mizinda yotetezedwa),   
10 inu mumadana ndi amene amadzudzula mʼbwalo la milandu  
ndi kunyoza amene amanena zoona.   
   
 
11 Mumapondereza munthu wosauka  
ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu.  
Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema,  
inuyo simudzakhalamo.  
Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa,  
inu simudzamwa vinyo wake.   
12 Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu  
ndi kukula kwa machimo anu.  
   
 
Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu  
ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.   
13 Nʼchifukwa chake pa nthawi yotere munthu wanzeru sayankhulapo kanthu,  
popeza ndi nthawi yoyipa.   
   
 
14 Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa,  
kuti mukhale ndi moyo.  
Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu,  
monga mmene mumanenera kuti ali nanu.   
15 Mudane ndi zoyipa, mukonde zabwino;  
mukhazikitse chiweruzo cholungama mʼmabwalo anu amilandu.  
Mwina mwake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzachitira chifundo  
anthu otsala a mʼbanja la Yosefe.   
16 Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena:  
“Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula,  
ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse.  
Adzayitana alimi kuti adzalire,  
ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula.   
17 Mʼminda yonse ya mpesa mudzakhala kulira kokhakokha,  
pakuti Ine ndidzadutsa pakati panu,”  
akutero Yehova.   
Tsiku la Yehova 
 
18 Tsoka kwa inu amene mumalakalaka  
tsiku la Yehova!  
Chifukwa chiyani mumalakalaka tsiku la Yehova?  
Tsikulo kudzakhala mdima osati kuwala.   
19 Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango  
amakumana ndi chimbalangondo,  
ngati pamene munthu walowa mʼnyumba,  
natsamira dzanja lake pa khoma  
ndipo njoka nʼkuluma.   
20 Kodi tsiku la Yehova silidzakhala mdima osati kuwala,  
mdima wandiweyani, popanda powala pena paliponse?   
   
 
21 “Ndimadana nawo masiku anu achikondwerero ndipo ndimawanyoza;  
sindikondwera nayo misonkhano yanu.   
22 Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya,  
Ine sindidzazilandira.  
Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano,  
Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe.   
23 Musandisokose nazo nyimbo zanu!  
Sindidzamvetsera kulira kwa azeze anu.   
24 Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi,  
chilungamo ngati mtsinje wosaphwa!   
   
 
25 “Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja  
munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?   
26 Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu,  
ndi nyenyezi ija Kaiwani,  
mulungu wanu,  
mafano amene munadzipangira.   
27 Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,”  
akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.