16
Timoteyo Atsagana ndi Paulo ndi Sila
1 Paulo anafika ku Derbe ndi Lusitra, kumene kumakhala ophunzira wina dzina lake Timoteyo. Amayi ake anali Myuda wokhulupirira, koma abambo ake anali Mgriki.
2 Abale a ku Lusitra ndi Ikoniya anamuchitira iye umboni wabwino.
3 Paulo anafuna kumutenga pa ulendo, kotero anachita mdulidwe chifukwa cha Ayuda amene amakhala mʼderalo pakuti onse amadziwa kuti abambo ake anali Mgriki.
4 Pamene amayenda mzinda ndi mzinda, amafotokoza zimene atumwi ndi akulu ampingo ku Yerusalemu anagwirizana kuti anthu azitsatire.
5 Kotero mipingo inalimbikitsidwa mʼchikhulupiriro ndipo anthu amachulukirachulukirabe tsiku ndi tsiku.
Paulo Awona Masomphenya
6 Paulo ndi anzake anadutsa mayiko a Frugiya ndi Galatiya, Mzimu Woyera atawaletsa kulalikira Mawu a Mulungu ku Asiya.
7 Atafika ku malire a Musiya, anayesa kulowa ku Bituniya, koma Mzimu wa Yesu sunawalole kutero.
8 Ndipo iwo anadutsa Musiya ndipo anapita ku Trowa.
9 Nthawi ya usiku Paulo anaona masomphenya, munthu wa ku Makedoniya atayimirira ndi kumupempha kuti, “Bwerani ku Makedoniya, mudzatithandize.”
10 Paulo ataona masomphenyawa, tinakonzeka kupita ku Makedoniya, kutsimikiza kuti Mulungu anatiyitana kuti tikalalikire Uthenga Wabwino.
Lidia Atembenuka Mtima ku Filipi
11 Kuchokera ku Trowa tinakwera sitima ya pamadzi kupita ku Samotrake ndipo mmawa mwake tinapitirira mpaka ku Neapoli.
12 Kuchokera kumeneko tinapita ku Filipi, boma la Aroma ndiponso mzinda waukulu wa dera la Makedoniya. Tinakhala kumeneko masiku owerengeka.
13 Pa tsiku la Sabata tinatuluka mu mzindawo kupita ku mtsinje kumene timayembekezera kukapeza malo opempherera. Tinakhala pansi ndipo tinayamba kuyankhula ndi amayi amene anasonkhana pamenepo.
14 Mmodzi wa amayi amene amamvetserawo ndi Lidiya amene amagulitsa nsalu zofiira, wochokera ku mzinda wa Tiyatira, ndipo amapembedza Mulungu. Ambuye anatsekula mtima wake kuti amve mawu a Paulo.
15 Iye ndi a mʼbanja lake atabatizidwa, anatiyitana kuti tipite ku nyumba yake. Iye anati, “Ngati mwanditenga ine kukhala wokhulupirira mwa Ambuye, bwerani mudzakhale mʼnyumba mwanga.” Ndipo anatiwumiriza ife kwambiri.
Paulo ndi Sila Mʼndende
16 Tsiku lina pamene timapita kumalo wopempherera, tinakumana ndi mtsikana wina amene anali ndi mzimu woyipa umene umanena zamʼtsogolo. Iye amapezera ndalama zambiri ambuye ake pa ulosi wake.
17 Mtsikanayu anatsatira Paulo ndi ife, akufuwula kuti, “Anthu awa ndi atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, amene akukuwuzani inu njira yachipulumutso.”
18 Iye anachita izi masiku ambiri. Kenaka Paulo anavutika mu mtima, natembenuka ndipo anati kwa mzimuwo, “Ndikukulamula iwe mʼdzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa iye!” Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.
19 Pamene ambuye a mtsikana uja anazindikira kuti chiyembekezo chawo chopezera ndalama chatha, anagwira Paulo ndi Sila nawakokera ku bwalo la akulu.
20 Anawabweretsa iwo kwa oweruza milandu ndipo anati, “Anthu awa ndi Ayuda, iwo akuvutitsa mu mzinda wathu.
21 Ndipo akuphunzitsa miyambo imene ife Aroma sitiloledwa kuyilandira kapena kuyichita.”
22 Gulu la anthu linatsutsana ndi Paulo ndi Sila, ndipo woweruza milandu analamula kuti avulidwe ndi kumenyedwa.
23 Atawakwapula kwambiri anawaponya mʼndende, nalamula woyangʼanira kuti awasunge mosamalitsa.
24 Chifukwa cha mawu amenewa woyangʼanira ndende anakawayika mʼchipinda chamʼkati mwa ndende, nawamangirira miyendo yawo mʼzigologolo.
25 Koma pakati pa usiku Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuyimba nyimbo zolemekeza Mulungu, ndipo akayidi ena ankamvetsera.
26 Mwadzidzidzi kunachitika chivomerezi champhamvu kotero kuti maziko a ndende anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse za ndende zinatsekuka, ndipo maunyolo a aliyense anamasuka.
27 Woyangʼanira ndende uja atadzuka ku tulo, anaona kuti zitseko za ndende zinali zotsekula, ndipo anasolola lupanga lake nafuna kudzipha chifukwa ankaganiza kuti amʼndende athawa.
28 Koma Paulo anafuwula kuti, “Usadzipweteke! Tonse tilipo!”
29 Woyangʼanira ndendeyo anayitanitsa nyale, nathamangira mʼkati ndipo anadzigwetsa pa mapazi a Paulo ndi Sila akunjenjemera.
30 Iye anawatulutsa kunja ndipo anawafunsa kuti, “Amuna inu, ndichite chiyani kuti ndipulumuke?”
31 Iwo anayankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako.”
32 Kenaka analalikira mawu a Ambuye kwa iyeyo ndi onse amene anali mʼnyumba mwake.
33 Usiku womwewo woyangʼanira ndendeyo anawatenga nakawatsuka mabala awo; ndipo pomwepo iye ndi a mʼbanja lake anabatizidwa.
34 Woyangʼanira ndendeyo anapita nawo ku nyumba yake, nakawapatsa chakudya, ndipo banja lonse linadzazidwa ndi chimwemwe chifukwa anakhulupirira Mulungu.
35 Kutacha, woweruza milandu uja anatuma asilikali kwa woyangʼanira ndendeyo kukanena kuti, “Amasuleni anthu aja.”
36 Woyangʼanira ndendeyo anawuza Paulo kuti, “Woweruza milandu walamula kuti iwe ndi Sila mumasulidwe. Tsopano muzipita. Pitani mumtendere.”
37 Koma Paulo anati kwa asilikaliwo: “Iwo anatikwapula pa gulu la anthu asanatiweruze, ngakhale kuti ndife nzika za Chiroma natiponya mʼndende. Kodi tsopano akufuna kutitulutsa mwamseri? Ayi! Asiyeni abwere okha kuti adzatitulutse.”
38 Asilikali aja anakafotokozera woweruza milandu ndipo pamene anamva kuti Paulo ndi Sila anali nzika za Chiroma, anachita mantha.
39 Iye anabwera kudzawapepesa ndipo anawatulutsa mʼndende, nawapempha kuti achoke mu mzindawo.
40 Paulo ndi Sila atatuluka mʼndende, anapita ku nyumba ya Lidiya, kumene anakumana ndi abale nawalimbikitsa. Kenaka anachoka.